Romans 1:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu amaŵakwiyira, chifukwa zimene munthu angathe kudziŵa zokhudza Mulungu iwo akuzidziŵa bwino lomwe, popeza kuti Mulungu mwini ndiye adaŵaululira zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chodziwika cha Mulungu chaonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa codziwika ca Mulungu caonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anacionetsera kwa iwo.