Romans 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;