Romans 1:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Mulungu anawasiya kuti azingochita zilakolako zochititsa manyazi zauchimo zomwe mitima yawo inkafuna. Zotsatira zake anachita za chiwerewere wina ndi mnzake kunyazitsa matupi awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kucititsana matupi ao wina ndi mnzace zamanyazi;