Romans 1:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici Mulungu anawapereka iwo 1 ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa macitidwe ao a cibadwidwe akhale macitidwe osalingana ndi cibadwidwe: