Romans 1:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimodzimodzinso amuna analeka machitidwe a ukwati ndi akazi nʼkumakhumbana amuna okhaokha. Amuna ankachita zochitisa manyazizi ndi amuna anzawo, ndipo analandira chilango choyenera molingana ndi zochita zawo zachitayikozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo cimodzimodzinso amuna anasiya macitidwe a cibadwidwe ca akazi, natenthetsana ndi colakalaka cao wina ndi mnzace, amuna okhaokha anacitirana camanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.