Romans 1:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;