Romans 10:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ntafunsa: kodi ndiye kuti Aisraele sadaŵamve mauwo? Iyai, kumva adamva ndithu. Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Liwu lao lidamveka pa dziko lonse lapansi, mau ao adafika mpaka ku malekezero a dziko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linaturukira ku dziko lonse lapansi, Ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.