Romans 10:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntafunsanso: monga nkuti Aisraele sadaŵamvetse mauwo? Mose ndiye woyamba kuyankhapo. Iye adati, “Ndidzakuchititsani kaduka ndi mtundu umene suli mtundu weniweni, ndidzakukwiyitsani ndi mtundu wa anthu opusa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nditi, Kodi Israele alibe kudziwa? Poyamba Mose anena, Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu, ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti, “Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake. Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nditi, Kodi Israyeli alibe kudziwa? Poyamba Mose anena, Ine ndidzacititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu, Ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.