Romans 10:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za chilungamo chimene chimapezeka pakumvera Malamulo, Mose adalemba kuti, “Munthu wochita zimene Malamulo amanena, adzakhala ndi moyo pakuzichita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m'lamulo, adzakhala nacho ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Mose walemba kuti munthu amene acita cilungamo ca m'lamulo, adzakhala naco ndi moyo.