Romans 11:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati munthu apatulira Mulungu chigawo chimodzi cha buledi, ndiye kuti yenseyo ndi wopatulika. Ndipo ngati muzu wa mtengo ndi wopatulika, ndiye kuti ndi nthambi zake zomwe nzopatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati zoundukula zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati chigawo chimodzi cha buledi woperekedwa monga zipatso zoyamba ndi choyera, ndiye kuti zonsezo ndi zoyera. Ngati muzu ndi oyera, nʼchimodzimodzinso nthambi zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati zoundukula ziri zopatulika, coteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, coteronso nthambi.