Romans 11:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthambi zina za mtengo wobzala wa olivi zidakadzuka, ndipo pamalo pa nthambi zimenezo adalumikizapo kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo. Ndiye kuti inu amene simuli Ayuda, muli ngati kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo uja, ndipo tsopano mukulandira nao mphamvu ya m'mizu ya mtengo wobzala wa olivi, ndiye kuti Ayuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wa kuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati nthambi zina zinakhadzulidwa ndipo inu, inu ndiye nthambi za olivi wakuthengo, nʼkulumikizidwa pamalo pa nthambi zimenezo, ndipo tsopano mukulandira nawo zakudya zochokera ku mizu ya olivi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wa kuthengo, unamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ace a mtengowo,