Romans 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu sadaŵataye anthu ake amene Iye adaŵasankha kale. Monga simudziŵa mau aja a m'Malembo, pamene mneneri Eliya akudandaula kwa Mulungu kuti aŵalange Aisraele? Paja adati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu sanataya anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu sanataya anthu ace amene iye anawadziwiratu, Kapena simudziwa kodi cimene lembo linena za Eliya? kuti anaumirira Mulungu poneneza Israyeli, kuti,