Romans 11:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nzoona, iwo adakadzukadi chifukwa sadakhulupirire, ndipo inu pakukhulupirira, mukukhala mu mtengo tsopano. Komatu tsono musamadzitame, makamaka muzichita mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼzoona. Koma iwo anakhadzulidwa chifukwa chosakhulupirira ndipo inu mukuyima mwachikhulupiriro. Musadzitukumule, koma muchite mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi cikhulupiriro cako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu: