Romans 11:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo zindikirani kuti Mulungu ndi wachifundodi, komanso ndi waukali. Kwa anthu amene adagwa, ndi wokwiya, koma kwa inu ndi wachifundo, malinga mukasamala chifundo chake. Ngati simuchita zimenezi, adzakudulani inunso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace onani cifatso ndi kuuma mtima kwace kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwace; koma kwa iwe cifatso cace ca Mulungu, ngati ukhala cikhalire m'eifatsomo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.