Romans 11:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu, amene muli nthambi ya mtengo wa olivi wakuthengo, Mulungu adakukadzulani ku mtengo umene udaakubalani, nakulumikizani ku mtengo wa olivi wobzala. Ngati zili choncho, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuti alumikizenso ku mtengo wa olivi wobzala, nthambi zakezake zimene zidakadzuka?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati iwe unasadzidwa ku mtengo wazitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unamezetsanidwa ndi mtengo wazitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wace, adzamezetsanidwa ndi mtengo wao womwewo wazitona?