Romans 11:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali chinsinsi, chimene ndifuna kuti muchidziŵe, kuwopa kuti mungamadziyese anzeru. Chinsinsicho ndi chakuti Aisraele ena adzapulupudza, mpaka nthaŵi imene chiŵerengero cha akunja otembenukira kwa Mulungu chidzakwanire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa za chinsinsi ichi, kuti mungadziyese nokha anzeru. Kuwuma mtima kumene Aisraeli akuchita ndi kwa kanthawi kufikira chiwerengero cha a mitundu chitalowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa cinsinsi ici, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israyeli, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;