Romans 11:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chokana Uthenga Wabwino, Ayuda asanduka adani a Mulungu, kuti inu mupindulepo. Koma ngati Mulungu adaŵasankha, iwo ndi abwenzi ake chifukwa cha makolo ao akale aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, cifukwa ca inu; koma kunena za cisankhidwe, z ali okondedwa, cifukwa ca makolo.