Romans 12:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;