Romans 12:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, acite ndi kukondwa mtima.