Romans 13:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Olamulira sachititsa mantha anthu a makhalidwe abwino, koma a makhalidwe oipa. Kodi ufuna kukhala wosaopa wolamulira? Uzichita zolungama, ndipo iye adzakuyamikira,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti olamulira saopseza amene amachita zabwino koma amene amachita zoyipa. Kodi mukufuna kukhala osaopa olamulira? Tsono chitani zoyenera ndipo adzakuyamikirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mafumu sakhala oopss nchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro: Cita cabwino, ndipo udzalandirs kutama m'menemo: