Romans 13:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokuchitirani zabwino. Koma ngati muchita zoyipa muchite mantha, pakuti iye ali ndi mphamvu zolangira. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wobweretsa mkwiyo ndi kulanga onse ochita zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kucitira iwe zabwino. Koma ngati ucita coipa opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwacabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwe zera cilango wocita zoipa.