Romans 13:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ili, Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.