Romans 14:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye amene ali wofoka m'cikhulupiriro, mumlandire, koma si kucita naye makani otsutsana ai.