Romans 14:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mʼbale wako akuvutika chifukwa cha chimene umadya, iwe sukuchitanso mwachikondi. Usamuwononge mʼbale wako amene Khristu anamufera chifukwa cha chakudya chakocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati iwe wacititsa mbale wako cisoni ndi cakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi cikondano. Usamuononga ndi cakudya cako, iye amene Kristu adamfera.