Romans 14:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musawononge ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Chakudya chonse ndi choyera, koma munthu amalakwa ngati adya chilichonse chimene chimakhumudwitsa wina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usapasule nchito ya Mulungu cifukwa ca cakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.