Romans 14:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu amene akukayika atsutsidwa ngati adya, chifukwa kudya kwake si kwa chikhulupiriro; ndipo chilichonse chosachokera mʼchikhulupiriro ndi tchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye amene akayika-kayika pakudya, atsutsika, cifukwa akudya wopanda cikhulupiriro; ndipo cinthu ciri conse cosaturuka m'cikhulupiriro, ndico ucimo.