Romans 14:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzake; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu aliyense akhazikike konse mumtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina amayesa tsiku limodzi lopatulika kuposa lina. Munthu wina amayesa masiku onse ofanana. Aliyense akhale otsimikiza mʼmaganizo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzace; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu ali yense akhazikike konse mumtima mwace.