Romans 15:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso Yesaya akuti, “Muzu wa Yese udzaphuka, wina amene adzauka kulamulira anthu a mitundu ina; mwa Iye mudzakhala chiyembekezo cha a mitundu ina.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Jese, Ndi iye amene aukira kucita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.