Romans 15:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,