Romans 15:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku onse ndinkayesetsa kulalika Uthenga Wabwino kumalo kokhako kumene dzina la Khristu linali lisanamvekebe. Ndinkaopa kumanga pa maziko amene munthu wina adaika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Khristu asanatchulidwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.