Romans 15:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndikuyembekeza kudzakuwonani pamene ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya. Ndidzakondwera kukuchezerani masiku angapo, ndipo pambuyo pake ndifuna kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamene paliponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukonza kuti nditero pamene ndipita ku Spaniya. Ine ndikuyembekeza kudzakuchezerani pamene ndikudutsa ndi kuti inu mudzathandize popitiriza ulendo wanga, nditasangalala ndi kukhala nanu kwa kanthawi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamene pali ponse ndidzapita ku Spanya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.