Romans 15:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde unali ufulu kuchita zimenezi, komanso unali udindo wao kuthandiza osaukawo. Ayuda adagaŵana madalitso ao achikhristu ndi anthu a mitundu ina, choncho iwowo ayeneranso kuthandiza Ayudawo pa zosoŵa zao za moyo wathupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo chinawakomera kuchita ichi, ndipo ndithu anali ndi ngongole kwa iwo. Pakuti ngati a mitundu ina anagawana ndi Ayuda madalitso auzimu, iwo ali ndi ngongole kwa Ayuda kuti agawane nawo madalitso awo a ku thupi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. 3 Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikica iwo ndi zinthu zathupi.