Romans 15:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nditatsiriza ntchito yangayi, ndi kutula bwino lomwe kwa iwo zoperekazi, ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzapyola kwanu kupita ku Spaniya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ine nditamaliza ntchito iyi ndi kutsimikiza kuti alandira chipatsochi, ndidzadzera kwanuko kudzakuchezerani pa ulendo wanga popita ku Spaniya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene ndikatsiriza ici, ndi kuwasindikizira iwo cipatso ici, ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.