Romans 15:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adaŵalonjeza makolo ao akale aja,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa kunena zoona, Khristu wasanduka mtumiki wa Ayuda, kuonetsa kuti Mulungu ndi wokhulupirika pa malonjezo amene anachita kwa makolo awo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,