Romans 15:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti a mitundu ina atamande Mulungu chifukwa cha chifundo chake. Monga kwalembedwa kuti, “Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa a mitundu; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa ca cifundo; monga kwalembedwa, Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, Ndidzayimbira dzina lanu.