Romans 16:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Moni kwa Trifena ndi Trifosa, amene amagwira mwamphamvu ntchito ya Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwa uja, amene wachita zambiri pogwirira Ambuye ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Moni kwa Trifena, ndi Trifosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwayo amene anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika. Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulankhule Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa nchito mwa Ambuyeo Mulankhule. Persida, wokondedwayo amene anagwiritsa nchito zambiri mwa Ambuye.