Romans 16:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndikudandaulirani; abale, yang'anirani iwo akucita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi ciphunzitsoco munaciphunzira inu; ndipopotolokani pa iwo.