Romans 16:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asoceretsamitiina ya osalakwa.