Romans 16:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlandireni m'dzina la Ambuye, monga momwe anthu a Mulungu ayenera kulandirirana. Mumthandize monga momwe angasoŵere chithandizo chanu, pakuti iyeyo adathandiza anthu ambiri, ine ndemwenso adandithandizako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zili zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.