Romans 16:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyeni tilemekeze Mulungu! Iye ali ndi mphamvu za kukulimbitsani potsata Uthenga Wabwino umene ndimaulalika, umene ndi mau olengeza za Yesu Khristu. Zimenezi zinali zachinsinsi, ndipo zidaabisika pa zaka zonse kuyambira kalekale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kwa iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa uthenga wanga wabwino, ndi kulalildra kwa Yesu Kristu, monga mwa bvumbulutso la cinsinsi cimene cinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,