Romans 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akucita lamulo adzayesedwa olungama,