Romans 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene sali Ayuda alibe Malamulo, koma pamene mwa iwo okha amachita zimene Malamulowo anena, amaonetsa kuti ali nawo malamulo mumtima mwao, ngakhale alibe Malamulo a Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu, pamene a mitundu ina, amene alibe Malamulo, koma mwachikhalidwe chawo amachita zimene zili mʼMalamulo, iwowo ndi Malamulo pa iwo okha, ngakhale kuti alibe Malamulowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amacita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;