Romans 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchito zaozo zimatsimikiza kuti Malamulowo ndi olembedwa m'mitima mwao. Mitima yao yomwe imatsimikiza kuti ndi momwemodi, popeza kuti maganizo ao m'chikatikati mwina amaŵatsutsa, mwina amaŵavomereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbu mtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito zawo zimaonetsa kuti Malamulowo alembedwa mʼmitima mwawo. Chikumbumtima chawonso chimawachitira umboni pakuti maganizo awo amawatsutsa kapena kuwavomereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;