Romans 2:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga iwe wonena kuti, “Osamachita chigololo,” bwanji iwenso umachita chigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, bwanji umaba za m'nyumba zopembedzeramo mafanowo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'Kachisi kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi iwe amene umanena kuti anthu asachite chigololo, umachitanso chigololo? Kodi iwe amene umanyasidwa ndi mafano, umalandanso za mʼnyumba zopembedzera mafanowo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe wakunena kuti munthu asacite cigololo, kodi umacita cigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'kacisi kodi?