Romans 2:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake wosaumbalayo amene amatsata Malamulo ndiye adzakutsutsa iwe amene uli woumbala, ndipo uli ndi Malamulo olembedwa, koma umaŵaphwanya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu amene sanachite mdulidwe mʼthupi koma amamvera Malamulo adzakutsutsa iwe wosamvera Malamulowe, ngakhale kuti uli nawo Malamulo olembedwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa cibadwidwe, ngati kukwanira cilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?