Romans 2:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Myuda weniwenitu ndi amene ali Myuda mumtima mwake, ndipo kuumbala kwenikweni ndi kwa mtima, kochitika ndi Mzimu Woyera, osati ndi Malamulo olembedwa ai. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwace sikucokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.