Romans 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tikudziŵa kuti zonse zimene Malamulo a Mulungu anena, zimakhalira amene ali olamulidwa ndi Malamulowo. Cholinga chake nchakuti anthu onse asoŵe ponena, ndipo onse adzazengedwe ndi Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tidziwa kuti zinthu ziri zonse cizinena cilamulo cizilankhulira iwo ali naco cilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;