Romans 3:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene Mulungu anamuika poyera akhale cotetezera mwa cikhulupiriro ca m'mwazi wace, kuti aonetse cilungamo cace, popeza Mulungu m'kulekerera kwace analekerera macimo ocitidwa kale lomwe;