Romans 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mpang'ono pomwe. Koma anthu adziŵe kuti zimene Mulungu amalankhula nzoonadi, ngakhale kuti anthu onse ndi onama. Ndi monga Malembo akunenera kuti, “Inu Mulungu, anthu adziŵe kuti mumanena zoona mukamalankhula, adziŵe kuti mumapambana mukamazenga mlandu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti, “Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi kupambana pamene muweruza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, Ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.