Romans 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo bwanji sitingonena kuti, “Tizichita zoipa kuti zabwino ziwoneke”? Alipo anthu ena amene amatisinjirira kuti timanena zotere. Iwoŵa adzalangidwa monga kuyenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tilekerenji kunena, Ticite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.